Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 11:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala mu Yudeya;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Pamenepo Akhristu aja adatsimikiza zotumiza thandizo kwa abale okhala ku Yudeya, ndipo kuti aliyense atumize molingana ndi kupata kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 11:29
27 Mawu Ofanana  

Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina ya siliva zikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi.


Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.


Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri.


Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo.


Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),


Koma atumwi ndi abale akukhala mu Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.


ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.


Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.


Koma pamene anamzinga ophunzirawo, anauka iye, nalowa m'mzinda; m'mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;


Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa,


Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.


ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.


koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.


sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;


pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa