Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 11:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala mu Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala m'Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mpingo wa ku Yerusalemu utamva zimene zidachitikazo, udatuma Barnabasi ku Antiokeyako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 11:22
16 Mawu Ofanana  

Koma atumwi ndi abale akukhala mu Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.


Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.


Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.


Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.


Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.


Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:


Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;


Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.


Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa.


Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa