Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 11:17 - Buku Lopatulika

17 Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Tsono ngati Mulungu adaŵapatsa iwowo mphatso yomweyo imene adapatsa ifeyo pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, nanga ine ndine yani kuti ndikadatha kumletsa Mulungu?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 11:17
14 Mawu Ofanana  

Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji? Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.


Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse? Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.


Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?


Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.


koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa