Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 11:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nthaŵi yomweyo kudafika anthu atatu kunyumba kumene ndinkakhala. Adaatumidwa kwa ine kuchokera ku Kesareya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Nthawi yomweyo anthu atatu amene anatumidwa kuchokera ku Kaisareya anayima pa nyumba yomwe ndimakhalayo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 11:11
7 Mawu Ofanana  

Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.


Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa Munthu ndiye yani?


Ndipo ichi chinachitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa