Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo m'mawa mwake analowa mu Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo m'mawa mwake analowa m'Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 M'maŵa mwake adafika ku Kesareya. Kornelio ankaŵadikira, atasonkhanitsa abale ndi abwenzi ake apamtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:24
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.


Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.


Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.


Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa Munthu ndiye yani?


Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao.


Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa