Machitidwe a Atumwi 10:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Iwo adati, “Kornelio, mkulu wa gulu la asilikali 100, watituma. Iyeyo ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu, ndipo Ayuda onse amamtama. Mngelo wa Mulungu adamuuza kuti akuitaneni kuti mupite kunyumba kwake akamve mau amene muli nawo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.” Onani mutuwo |