Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:20 - Buku Lopatulika

20 Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Nyamuka, tsika, upite nawo osakayika, pakuti ndaŵatuma ndine.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:20
11 Mawu Ofanana  

Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.


Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.


Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; chifukwa chake mwadzera nchiyani?


Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;


Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Seleukiya; ndipo pochokerapo anapita m'ngalawa ku Kipro.


Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.


Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;


Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa