Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pamene Petro ankalingalirabe za zimene adaaziwona m'masomphenya zija, Mzimu Woyera adamuuza kuti, “Iwe, anthu atatu akukufuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:19
11 Mawu Ofanana  

Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.


ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wotchedwanso Petro, acherezedwako.


Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.


Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.


Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.


Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu.


Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna.


Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa