Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Petro adayamba kusinkhasinkha za tanthauzo la zimene adaaziwona m'masomphenya zija. Nthaŵi yomweyo anthu amene Kornelio adaaŵatuma aja, ankafunsa za nyumba ya Simoni, ndipo tsopano adaadzaima pa khomo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:17
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi?


Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.


Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?


Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi.


Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.


Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,


Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.


ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa