Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:10 - Buku Lopatulika

10 koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ali pamenepo, adamva njala, namafuna kudya. Koma pamene anthu ankakonza chakudya, iye adachita ngati wakomoka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:10
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.


M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israele, nandikhalitsa paphiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mzinda kumwera.


anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.


wakumva mau a Mulungu anenetsa, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.


Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala.


Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.


Ndinali ine m'mzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine;


Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,


Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa