Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:17 - Buku Lopatulika

17 Chifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lake la utumiki uwu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Chifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lake la utumiki uwu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Yudasiyo anali mmodzi wa gulu lathu, ndipo adaalandira udindo woti azitumikira pamodzi ndi ife.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:17
13 Mawu Ofanana  

Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye.


ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye. Ndipo analowa m'nyumba.


Pamene Iye anali chilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona Iye.


ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye.


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.


Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.


Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka;


Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa