Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:14 - Buku Lopatulika

14 Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:14
27 Mawu Ofanana  

Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.


Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.


Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patali, omwe anatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye;


Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;


Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.


Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?


Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;


Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi.


Ndipo akazi, amene anachokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wake.


Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.


Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi,


ndipo anakhala chikhalire mu Kachisi, nalikuyamika Mulungu. Amen.


Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu.


Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.


Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.


Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;


Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.


kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.


Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.


mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa