Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 23:31 - Buku Lopatulika

31 Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Pakuti ngati mtengo wauŵisi auchita zimenezi, nanga mtengo wouma ndiye adzauchita zotani?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:31
13 Mawu Ofanana  

Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno; koposa kotani woipa ndi wochimwa?


Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mzinda umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.


Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ochita zoipa, anatengedwa pamodzi ndi Iye kuti aphedwe.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.


Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa