Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 23:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Adaŵamasulira munthu amene ankamupempha uja, amene adaaponyedwa m'ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu. Koma Yesu adampereka kwa iwo kuti akamchite zimene ankafuna.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:25
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu idati kwa Hamani, siliva akhale wako, ndi anthu omwe; uchite nao monga momwe chikukomera.


Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.


Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.


Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.


Ndipo Pilato anaweruza kuti chimene alikufunsa chichitidwe.


Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.


Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.


Pomwepo anafuulanso, nanena, Si uyu, koma Barabasi. Koma Barabasi anali wachifwamba.


Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Pamenepo anatenga Yesu;


Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,


Chifukwa chake siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa