Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 23:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeze chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pilato adaŵafunsa kachitatu kuti, “Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:22
8 Mawu Ofanana  

nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeze pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;


Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye.


Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;


koma iwo anafuula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni pamtanda.


Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo mau ao anapambana.


Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa