Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 23:14 - Buku Lopatulika

14 nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeze pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Adaŵauza kuti, “Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokeza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:14
10 Mawu Ofanana  

Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.


nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.


Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


Ndipo ngakhale sanapeze chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.


Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa