Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 20:46 - Buku Lopatulika

46 Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 “Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero ndiponso malo olemekezeka pa maphwando.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 “Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando.

Onani mutuwo Koperani




Luka 20:46
14 Mawu Ofanana  

Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.


Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ake,


Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.


Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika.


Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.


Ndipo Iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,


amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero aatali; amenewo adzalandira kulanga koposa.


M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;


ameneyo iwenso uchenjere naye; pakuti anatsutsana nao mau athu.


Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa