Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 20:37 - Buku Lopatulika

37 Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Koma zakuti anthu adzauka kwa akufa, Mose yemwe adaanenapo kale. Paja pa mbiri ija ya chitsamba choyaka moto, iye akuŵatchula Ambuye kuti, ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 20:37
10 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.


Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;


kuti ndibwerenso kunyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga,


Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:


Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.


ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwake, ndi chivomerezo cha Iye anakhala m'chitsambayo. Mdalitso ufike pamutu wa Yosefe, ndi pakati pamutu wake wa iye wokhala padera ndi abale ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa