Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 20:17 - Buku Lopatulika

17 Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unakhala mutu wa pangodya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unakhala mutu wa pangodya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma Yesu adaŵayang'ana nati, “Nanga tsono tanthauzo lake nchiyani Malembo aŵa akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti, “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana wasanduka mwala wa pa ngodya.

Onani mutuwo Koperani




Luka 20:17
17 Mawu Ofanana  

Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya.


chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.


Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.


Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!


Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.


Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya.


omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;


Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika mu Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa