Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 2:46 - Buku Lopatulika

46 Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye m'Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso.

Onani mutuwo Koperani




Luka 2:46
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu.


Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.


Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.


Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israele, ndipo sudziwa izi?


Koma ananyamukapo wina pabwalo la akulu a milandu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa malamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.


pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa