Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 19:26 - Buku Lopatulika

26 Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:26
17 Mawu Ofanana  

koma chifundo changa sichidzamchokera iye, monga ndinachichotsera Saulo amene ndinamchotsa pamaso pako.


Masiku ake akhale owerengeka; wina alandire udindo wake.


Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.


Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako.


Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi.


Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi.


Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.


Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalimo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang'aniro wake autenge wina.


Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.


ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.


Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako.


Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa