Luka 15:29 - Buku Lopatulika29 Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwire lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatse ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Koma iye adayankha bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ndipo sindidalakwirepo lamulo lanu. Komabe inu simudandipatsepo ndi katonde komwe kuti ndikondwere pamodzi ndi anzanga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga. Onani mutuwo |