Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 15:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwanawang'ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwanawang'ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Iye adati, ‘Mng'ono wanu uja wabwera, ndiye bambo apha mwanawang'ombe wonenepa uja chifukwa amlandira ali wamoyo.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Iye anayankha kuti, ‘Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 15:27
8 Mawu Ofanana  

Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati.


Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?


Koma anakwiya, ndipo sanafune kulowamo. Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira.


Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang'ombe wonenepa.


anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.


Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.


Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa