Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 15:17 - Buku Lopatulika

17 Koma m'mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma m'mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 “Atakhalakhala adadzidzimuka mumtima mwake, ndipo adati, ‘Achulukirenji antchito a bambo wanga amene ali ndi chakudya chokwanira mpaka kutsalako, pamene ine kuno ndikufa ndi njala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala!

Onani mutuwo Koperani




Luka 15:17
19 Mawu Ofanana  

Ndinaganizira njira zanga, ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.


Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ntchafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, chifukwa ndinasenza chitonzo cha ubwana wanga.


M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire; pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake.


Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zake zonse adazichita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.


Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.


Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.


Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake.


Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.


Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.


Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?


Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa