Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 14:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Munthu wina amene ankadya nao, atamva zimenezi, adauza Yesu kuti, “Ngwodala munthu amene adzadye nao mu Ufumu wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 14:15
8 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.


Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Ndipo anthu adzachokera kum'mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu.


pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.


ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa