Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 13:33 - Buku Lopatulika

33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkucha, chifukwa sikuloleka kuti mneneri aonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkucha, chifukwa sikuloleka kuti mneneri aonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Komabe ndiyenera kupitirira ndi ulendo wanga lero ndi maŵa ndi mkucha, pakuti mneneri sangafere kwina koma ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:33
10 Mawu Ofanana  

Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,


Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu.


Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.


Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa