Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 12:35 - Buku Lopatulika

35 Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 “Khalani okonzeka kutumikira, ndipo nyale zanu zikhale zoyaka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 “Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka,

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:35
11 Mawu Ofanana  

Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.


Amanga m'chuuno mwake ndi mphamvu, nalimbitsa mikono yake.


Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.


palibe amene adzalema, kapena adzaphunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'chuuno mwao silidzamasuka, kapena chomangira cha nsapato zao sichidzaduka;


Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.


Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;


kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa