Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 12:33 - Buku Lopatulika

33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge.

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:33
14 Mawu Ofanana  

Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu; alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.


Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.


Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.


Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.


Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.


Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.


Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni mu Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.


Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.


Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.


kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa