Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 9:18 - Buku Lopatulika

18 Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza paguwa la nsembe pozungulira,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono adaphanso ng'ombe ndi nkhosa yamphongo, kuperekera anthu nsembe yachiyanjano. Pambuyo pake ana a Aroni adampatsira magazi, ndipo iye adathira magaziwo pa guwa molizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 9:18
7 Mawu Ofanana  

Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde paguwa la nsembe;


Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;


Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.


mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za mu Mwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa