Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 8:24 - Buku Lopatulika

24 Pamenepo anabwera nao ana aamuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo paguwa la nsembe pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pambuyo pake adabwera ndi ana a Aroni, ndipo Mose adapaka magazi pa nsonga za makutu ao a ku dzanja lamanja ndi pa zala zao zazikulu za ku dzanja lamanja, ndiponso pa zala zao zazikulu za ku phazi la ku dzanja lamanja. Kenaka Mose adathira magazi pa guwa molizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Pambuyo pake Mose anabwera ndi ana aamuna a Aaroni ndi kupaka magazi pa ndewere za makutu awo akumanja, pa zala zawo zazikulu za dzanja lamanja, ndiponso pa zala zawo zazikulu za kuphazi lakumanja. Kenaka iye anawaza magazi otsalawo mbali zonse za guwalo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:24
4 Mawu Ofanana  

Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;


Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa