23 Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja.
23 Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja.
23 Apo Mose adaipha, natengako magazi ake naŵapaka pa nsonga ya khutu la Aroni ku dzanja lamanja. Adapakanso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha ku phazi la dzanja lamanja.
23 Mose anayipha nkhosayo ndipo anatenga magazi ake ena ndi kupaka ndewere za khutu la kudzanja lamanja la Aaroni, pa chala chake chachikulu cha kudzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha phazi lakumanja.
Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.
Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.
Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;
ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula;
naphe mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;
ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pamalo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula;
Icho ndi chilamulo cha nsembe yopsereza, cha nsembe yaufa, cha nsembe yauchimo, ndi cha nsembe yopalamula, ndi cha kudzaza dzanja, ndi cha nsembe zoyamika;
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusaweruzika kuti zichite kusaweruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso.
kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala mu Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:
Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.