Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 8:21 - Buku Lopatulika

21 Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono atatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, adazitenthanso. Motero adatentha nkhosa yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma, yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, monga momwe Iye adaalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Anatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, ndi kutentha nkhosa yonseyo pa guwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yachakudya yoperekedwa kwa Yehova monga Yehovayo analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:21
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake.


Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.


Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa