Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 8:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pambuyo pake Mose adabwera ndi ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kenaka Mose anabwera ndi ngʼombe yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aaroni ndi ana ake anasanjika manja awo pamutu pa ngʼombeyo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:14
17 Mawu Ofanana  

Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang'ombe, akhale wa nsembe yauchimo.


Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.


Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova.


Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.


ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,


Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.


Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa