Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 8:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kenaka adabwera ndi ana a Aroni aja naŵaveka miinjiro, naŵamanga malamba m'chiwuno, ndi kuŵaveka zikofiya kumutu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kenaka anabwera ndi ana a Aaroni. Anawaveka minjiro, ndi kuwamanga malamba mʼchiwuno ndi kuwaveka nduwira kumutu monga momwe Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:13
15 Mawu Ofanana  

Ansembe anu avale chilungamo; ndi okondedwa anu afuule mokondwera.


Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.


Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.


Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawavula malaya ao a m'kati, kunka nao kunja kwa chigono, monga Mose adauza.


Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.


ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa