Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 8:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo anawazako paguwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Anawaza mafuta ena pa guwa kasanu ndi kawiri, nalidzoza guwalo pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso beseni ndi tsinde lake, nazipatula.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:11
13 Mawu Ofanana  

Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka.


Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.


Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.


Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.


Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.


Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo.


Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa.


momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova;


naviike chala chake m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, chakuno cha nsalu yotchinga.


ndipo wansembeyo aviike chala chake m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.


amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa