Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:27 - Buku Lopatulika

27 Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Munthu aliyense wophwanya lamulo limeneli, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Ngati munthu aliyense adya magazi achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:27
7 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


Pamenepo anauza Saulo, kuti, Onani anthu alikuchimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munachita konyenga; kunkhunizani mwala waukulu kwa ine lero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa