Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:25 - Buku Lopatulika

25 Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Pakuti munthu amene adya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Chauta kuti ikhale nsembe yotentha pamoto, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Pakuti munthu wakudya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe yotentha pa moto, ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:25
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.


Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse.


Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse.


Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa