Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:20 - Buku Lopatulika

20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Koma munthu woipitsidwa akadya nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Koma ngati munthu wina amene ndi wosayeretsedwa adya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:20
16 Mawu Ofanana  

Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.


Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?


Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wao.


koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.


Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko.


Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.


Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.


Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa