Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Kenaka atengeko mtanda umodzi pa mtundu uliwonse wa buledi, kuti ukhale nsembe yopereka kwa Chauta. Mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe zachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:14
10 Mawu Ofanana  

Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.


Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.


Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.


Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.


Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?


Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa