Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 6:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo moto wa paguwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo moto wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Moto wapaguwa uzikhala uli chiyakire, usazime. Wansembe azisonkhezera motowo ndi nkhuni m'maŵa mulimonse, ndipo aziyala nsembe yopsereza paguwapo, ndi kupserezapo mafuta a nsembe zachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 6:12
14 Mawu Ofanana  

ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.


Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.


Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.


Moto uziyakabe paguwa la nsembe, wosazima.


Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za paguwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa paguwa la nsembe uziyakabe pamenepo.


Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.


koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa