Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 6:11 - Buku Lopatulika

11 Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono avule zovala zake, avale zina, ndipo aole phulusalo nkukaliika pa malo oyeretsedwa kunja kwa mahema.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Akatero avule zovala zakezo ndi kuvala zovala zina. Kenaka atulutse phulusalo ndi kukaliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa chithando.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 6:11
14 Mawu Ofanana  

Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.


Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.


Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.


Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.


inde ng'ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.


Ndipo atulutse ng'ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.


Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.


Ndipo moto wa paguwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.


Chopereka cha Aroni ndi ana ake, chimene azibwera nacho kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ichi: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale chopereka chaufa kosalekeza, nusu lake m'mawa, nusu lake madzulo.


Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwake, wa mwa ana ake, achite ichi; likhale lemba losatha; achitenthe konse kwa Yehova.


Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa