Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 4:29 - Buku Lopatulika

29 Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa mbuzi ya nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aiphere pa malo amene amaperekera nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:29
10 Mawu Ofanana  

Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.


Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yauchimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao,


Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.


Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira paguwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.


Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.


naike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.


Naike dzanja lake pamutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza.


Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la chihema chokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa