Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 4:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo khamu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 “Ngati mpingo wonse wa Aisraele uchimwa mosachitira dala, nuchita zimene Chauta amaletsa, ngakhale uli wosadziŵako, ngwopalamula ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “ ‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:13
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzachotsa akazi ao; ndipo popeza adapalamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kupalamula kwao.


Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.


Ndipo tsiku lomwelo kalonga adzikonzere yekha ndi anthu onse a m'dziko ng'ombe, ikhale ya nsembe yauchimo.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo atulutse ng'ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.


Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.


pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;


Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;


Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.


ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;


Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa