Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 27:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ikakhala nyama yonga imene anthu amaperekera nsembe kwa Chauta, zonse zimene anthu amapereka kwa Chauta nzopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “ ‘Ngati chimene anachitira lumbiro kuti apereke ndi nyama imene amapereka kukhala nsembe kwa Yehova, zonse zimene amapereka kwa Yehova nʼzopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 27:9
7 Mawu Ofanana  

Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika, kuli msampha kwa munthu, ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.


Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?


Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti lili lopatulika la Yehova.


Asaisinthe, yokoma m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m'malo mwa inzake, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika.


Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.


Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m'gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula;


Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa