Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 27:8 - Buku Lopatulika

8 Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Munthu akakhala wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira mtengo umenewo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo aike mtengo pa iye. Mtengo umene wansembeyo aike ukhale wolingana ndi momwe munthu wolumbirayo angalipire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 27:8
11 Mawu Ofanana  

Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.


Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m'nyumba za adama.


Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.


Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi.


Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.


Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.


Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.


Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa