Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 27:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Munthu amene adapereka munda, akafuna kuti auwombole, pa mtengo wa mundawo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo udzakhala wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ngati munthu amene wapereka munda afuna kuwuwombola, ayenera kuwonjezera pa mtengo wake wa mundawo, limodzi mwa magawo asanu a mtengowo. Ndipo mundawo udzakhalanso wake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 27:19
4 Mawu Ofanana  

Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake.


Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.


Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.


Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa