Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 27:18 - Buku Lopatulika

18 Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Koma akapereka munda wake chitatha chaka chokondwerera zaka 50, wansembe aŵerenge mtengo wa ndalama molingana ndi zaka zotsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka 50, ndipo achotse pa mtengo umene wansembe waika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Koma ngati apereka mundawo chaka chokondwerera zaka makumi asanu chitapita, wansembe adzatchula mtengo molingana ndi zaka zomwe zatsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo mtengo wake udzakhala wotsikirapo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 27:18
7 Mawu Ofanana  

pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwake, nabwezere wogulayo zotsalirapo nabwerere iye ku dziko lake.


Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.


Akapatula munda wake kuyambira chaka choliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.


Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake.


pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wake wa kuyesa kwako kufikira chaka choliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, chikhale chinthu chopatulikira Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa