Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 26:22 - Buku Lopatulika

22 Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Popeza ndidzatumiza chilombo cha kuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nichidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ndidzabweretsanso zilombo zolusa pakati panu, zimene zidzakudyerani ana anu, ndi kukuwonongerani ng'ombe zanu. Zilombozo zidzachepetsa chiŵerengero chanu, kotero kuti m'njira zanu simuzidzapita anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:22
17 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaope Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.


Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.


Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo.


Chifukwa chake chitemberero chadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ochimwa, chifukwa chake okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala.


Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asiriya wathyola chipangano, wanyoza mizinda, sasamalira anthu.


Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.


nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;


M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.


Ndikapititsa zilombo zoipa pakati padziko, ndi kupulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo,


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.


Inde ndidzakutumizirani njala ndi zilombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndachinena.


Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.


Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.


Masiku a Samigara, mwana wa Anati, masiku a Yaele maulendo adalekeka ndi apanjira anayenda mopazapaza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa