Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 26:19 - Buku Lopatulika

19 Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndidzaononga nyonga zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale youma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:19
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Pamene kumwamba kwatsekera, ndipo kulibe mvula chifukwa cha kuchimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;


Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;


Ndipo iye adzatambasula manja ake pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ake posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwake, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ake.


Chifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mzinda wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi.


Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.


Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukulu kwa Yerusalemu.


Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.


Atero Yehova, Iwonso ochirikiza Ejipito adzagwa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatsika, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene adzagwa m'kati mwake ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.


Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.


Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.


Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;


ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zake; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani.


Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko lili pansi panu ngati chitsulo.


Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.


Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa