Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 25:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mulize lipenga mokweza. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo, ndilo tsiku limene mulize lipengalo m'dziko lanu lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri mulize lipenga mofuwula. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo muziliza lipenga mʼdziko lanu lonse.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 25:9
20 Mawu Ofanana  

Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m'chilungamo chanu.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m'dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.


Ndipo atatha kuchitira chotetezera malo opatulika, ndi chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;


Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzichepetsa, osagwira ntchito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;


popeza tsikuli adzachitira inu chotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukuchotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.


Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.


Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.


Akapatula munda wake kuyambira chaka choliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.


Chaka choliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lakelake.


Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo pofika chaka choliza cha ana a Israele adzaphatikiza cholowa chao ku cholowa cha fuko limene akhalako; chotero adzachotsa cholowa chao ku cholowa cha fuko la makolo athu.


Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.


mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;


Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati mu Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.


Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa